Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 19:14 - Buku Lopatulika

14 Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nizituma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Koma anthu ake ankadana naye, choncho m'mbuyo muno adatuma nthumwi kuti zipite ku dziko lomwelo nkukanena kuti, ‘Ife sitikufuna konse kuti munthu ameneyu akhale mfumu yathu.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 “Koma anthu ake anamuda ndipo anatuma nthumwi pambuyo pake kukanena kuti, ‘Sitikufuna munthuyu kuti akhale mfumu yathu.’

Onani mutuwo Koperani




Luka 19:14
15 Mawu Ofanana  

koma wakukhudza iyo adzikonzeratu chitsulo ndi luti la mkondo; ndipo idzatenthedwa konse ndi moto m'malo mwao.


Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.


Ndipo ndinatha abusa atatuwo mwezi umodzi; pakuti mtima wanga unalema nao, ndi mtima waonso unaipidwa nane.


Koma ngati sakhoza, atumiza akazembe, pokhala winayo ali kutalitali, nafunsa za mtendere.


Ndipo anaitana akapolo ake khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi za mina, nati kwaiwo, Chita nazoni malonda kufikira ndibweranso.


Ndipo kunali, pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo anapindulira pochita malonda.


Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.


Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamlandire Iye.


Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa