Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 19:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo kunali, pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo anapindulira pochita malonda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo kunali, pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo anapindulira pochita malonda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 “Komabe iye adalandira ufumu uja. Tsono atabwerera kwao, adaitanitsa antchito aja adaaŵapatsa ndalamaŵa kuti adziŵe zimene adapindula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 “Iye analandira ufumuwo ngakhale zinali zotero, ndipo anabwerera kwawo. Kenaka iye anatumiza uthenga kwa antchito ake amene anawapatsa ndalama aja, ndi cholinga chakuti adziwe chimene anapindula nazo.

Onani mutuwo Koperani




Luka 19:15
9 Mawu Ofanana  

Ndipo itapita nthawi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, nawerengera nao pamodzi.


Koma iye amene sanachidziwe, ndipo anazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.


Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.


Ndipo anafika woyamba, nanena, Mbuye, mina yanu inachita nionjeza mina khumi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa