Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

Masalimo 99 - Buku Lopatulika


Mulungu wamkulu wachifundo alemekezedwe

1 Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere; Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.

2 Yehova ndiye wamkulu mu Ziyoni; ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.

3 Alemekeze dzina lanu lalikulu ndi loopsa. Ili ndilo loyera.

4 Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo; Inu mukhazikitsa zolunjika, muchita chiweruzo ndi chilungamo mu Yakobo.

5 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, ndipo gwadirani poponderapo mapazi ake: Iye ndiye Woyera.

6 Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.

7 Iye analankhula nao mu mtambo woti njo: Iwo anasunga mboni zake ndi malembawa anawapatsa.

8 Munawayankha, Yehova Mulungu wathu: munawakhalira Mulungu wakuwakhululukira, mungakhale munabwezera chilango pa zochita zao.

9 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, ndipo gwadirani paphiri lake loyera; pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi
Titsatireni:



Zotsatsa