Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 99:6 - Buku Lopatulika

6 Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Mose ndi aroni anali ena mwa ansembe ake, Samuele nayenso anali mmodzi mwa anthu otama dzina la Chauta mopemba. Ankalira kwa Chauta Iye nkumaŵayankha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake, Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake; iwo anayitana Yehova ndipo Iyeyo anawayankha.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 99:6
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ufuuliranji kwa Ine? Lankhula ndi ana a Israele kuti aziyenda.


Ndipo iye anafuulira kwa Yehova; ndipo Yehova anamsonyeza mtengo ndipo anauponya m'madzimo, ndi madzi anasanduka okoma. Pamenepo anawapangira lemba ndi chiweruzo, ndi pomwepa anawayesa;


Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwachitenji anthuwa? Atsala pang'ono kundiponya miyala.


Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose anati kwa anthu, Mwachimwa kuchimwa kwakukulu; koma ndikwera kwa Yehova tsopano, kapena ndidzachita chotetezera uchimo wanu.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa