Yeremiya 5:22 - Buku Lopatulika22 Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Ine Chauta ndikuti, Kodi simukuchita nane mantha? Kodi simukunjenjemera pamaso panga? Ndine amene ndidaika mchenga kuti ukhale malire a nyanja, malire amene nyanjayo singaŵabzole. Mafunde ake, ngakhale aŵinduke bwanji, sangathe kupitirirapo. Ngakhale akokome chotani, sangathe kubzola. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Kodi simuyenera kuchita nane mantha?” Akutero Yehova. “Kodi simuyenera kunjenjemera pamaso panga? Ine ndinayika mchenga kuti ukhale malire a nyanja, malire a muyaya amene nyanjayo singadutsepo. Mafunde angawombe motani, koma sangathe kupitirira malirewo; mafunde angakokome motani, koma sangadutse malirewo. Onani mutuwo |
Chifukwa chanji ndinafika osapeza munthu? Ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? Pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja, ndi kusandutsa mitsinje chipululu; nsomba zake zinunkha chifukwa mulibe madzi, ndipo zifa ndi ludzu.