Pakuti ife ndife adzulo, osadziwa kanthu, popeza masiku athu a padziko lapansi ndiwo ngati mthunzi;
Masalimo 82:5 - Buku Lopatulika Sadziwa, ndipo sazindikira; amayendayenda mumdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sadziwa, ndipo sazindikira; amayendayenda mumdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo sadziŵa kanthu ndiponso alibe nzeru, amangoyenda m'chimbulimbuli. Maziko onse a dziko lapansi agwedezeka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse. Amayendayenda mu mdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka. |
Pakuti ife ndife adzulo, osadziwa kanthu, popeza masiku athu a padziko lapansi ndiwo ngati mthunzi;
Kodi onse ochita zopanda pake sadziwa kanthu? Pakudya anthu anga monga akudya mkate, ndipo saitana pa Yehova.
Kodi ochita zopanda pake sadziwa? Pomadya anthu anga monga akudya mkate; ndipo saitana Mulungu.
Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere; Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.
Wanzeru maso ake ali m'mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti chomwe chiwagwera onsewo ndi chimodzi.
Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zoipa; ndi malo a chilungamo, komweko kuli zoipa.
Chifukwa kuti munda wampesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israele, ndi anthu a Yuda, mtengo wake womkondweretsa; Iye nayembekeza chiweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza chilungamo, koma onani kufuula.
Chifukwa chake chiweruziro chili patali ndi ife, ndi chilungamo sichitipeza; tiyang'anira kuunika, koma taona mdima; tiyang'anira kuyera, koma tiyenda mu usiku.
Ndipo ndinati, Imvanitu, inu akulu a Yakobo, ndi oweruza a nyumba ya Israele; simuyenera kodi kudziwa chiweruzo?
Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako.
Koma chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza kudziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zao zinali zoipa.
Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;
Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.
Koma iye wakumuda mbale wake ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ake.