Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 12:35 - Buku Lopatulika

35 Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Apo Yesu adaŵauza kuti, “Kuŵala kukhalabe pakati panu, koma kanthaŵi pang'ono chabe. Yendani pamene kuŵalako kuli pakati panu, kuti mdima ungakugwereni. Munthu woyenda mu mdima saona kumene akupita.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Inu mukhala ndi kuwunika kwa nthawi pangʼono. Yendani pamene mukanali ndi kuwunika, kuti mdima usakupitirireni. Munthu amene amayenda mu mdima sadziwa kumene akupita.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 12:35
27 Mawu Ofanana  

Njira ya oipa ikunga mdima; sadziwa chimene chiwaphunthwitsa.


Inu a nyumba ya Yakobo, tiyeni, tiyende m'kuwala kwa Yehova.


Chifukwa chake njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzachotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.


Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita.


Koma ngati munthu ayenda usiku, akhumudwa, chifukwa mulibe kuunika mwa iye.


Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, chifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi.


Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako. Izi Yesu analankhula, nachoka nawabisalira.


Ndadza Ine kuunika kudziko lapansi, kuti yense wokhulupirira Ine asakhale mumdima.


Katsala kanthawi, ndipo simundionanso Ine, ndipo kanthawinso, ndipo mudzandiona Ine.


Pamenepo Yesu anati, Katsala kanthawi ndili ndi inu, ndipo ndimuka kwa Iye wondituma Ine.


Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.


koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa kuwerenga kwa pangano lakale chophimba chomwechi chikhalabe chosavundukuka, chimene chilikuchotsedwa mwa Khristu.


Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.


pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa