Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 2:14 - Buku Lopatulika

14 Wanzeru maso ake ali m'mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti chomwe chiwagwera onsewo ndi chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Wanzeru maso ake ali m'mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti chomwe chiwagwera onsewo ndi chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Inde munthu wanzeru amayenda maso ali patsogolo, pamene chitsiru chimayenda m'chimbulimbuli. Komabe ndidazindikira kuti zomwe zagwera winayo, mnzakeyonso zimamgwera zomwezo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Munthu wanzeru amayenda maso ali patsogolo, pamene chitsiru chimayenda mʼchimbulimbuli; koma ndinazindikira kuti chomwe chimawachitikira onsewo ndi chimodzi.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 2:14
16 Mawu Ofanana  

Ndizo zifunika koposa golide, inde, golide wambiri woyengetsa; zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake.


Pakuti aona anzeru amafa, monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo, nasiyira ena chuma chao.


Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala chikhalire, ndi mokhala iwo ku mibadwomibadwo; atchapo dzina lao padziko pao.


Nzeru ya wochenjera ndiyo yakuti azindikire njira yake; koma utsiru wa opusa ndiwo chinyengo.


Nzeru ili pamaso pa wozindikira; koma maso a wopusa ali m'malekezero a dziko.


Pakuti wanzeru saposa chitsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m'tsogolomo. Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati chitsirutu.


Pakuti chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe.


akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita kumalo amodzi?


Pakuti wanzeru ali ndi chiyani choposa chitsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pamaso pa amoyo ali ndi chiyani?


Kunka kunyumba ya maliro kupambana kunka kunyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.


Ndani akunga wanzeru? Ndani adziwa tanthauzo la mau? Nzeru ya munthu iwalitsa nkhope yake, kuduwa kwa nkhope yake ndi kusanduka.


Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake.


Pamenepo ndinati, Nzeru ipambana mphamvu; koma anyoza nzeru ya wosauka, osamvera mau ake.


Koma iye wakumuda mbale wake ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa