2 Timoteyo 2:19 - Buku Lopatulika19 Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Komabe maziko olimba, amene Mulungu adaŵaika, ngokhazikika, ndipo mau olembedwapo ndi aŵa: “Ambuye amadziŵa amene ali ao”, ndiponso, “Aliyense wotamanda dzina la Ambuye, asiye zosalungama.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Komabe maziko olimba, amene Mulungu anawayika ngokhazikika, ndipo mawu olembedwapo ndi awa: “Yehova amadziwa amene ndi ake,” ndiponso, “Aliyense amene amavomereza dzina la Ambuye ayenera kusiya zoyipa.” Onani mutuwo |
Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.