Masalimo 75 - Buku LopatulikaMulungu woweruza asiyanitsa pakati pa odzikuza ndi olungama Kwa Mkulu wa Nyimbo: Altasyeti. Salimo la Asafu. Nyimbo. 1 Tikuyamikani Inu, Mulungu; tiyamika, pakuti dzina lanu lili pafupi; afotokozera zodabwitsa zanu. 2 Pakuona nyengo yake ndidzaweruza molunjika. 3 Lasungunuka dziko lapansi, ndi onse okhalamo; ndinachirika mizati yake. 4 Ndinati kwa odzitamandira, musamachita zodzitamandira; ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga; 5 musamakwezetsa nyanga yanu; musamalankhula ndi khosi louma. 6 Pakuti kukuzaku sikuchokera kum'mawa, kapena kumadzulo, kapena kuchipululu. 7 Pakuti Mulungu ndiye woweruza; achepsa wina, nakuza wina. 8 Pakuti m'dzanja la Yehova muli chikho; ndi vinyo wake achita thovu; chidzala ndi zosakanizira, ndipo atsanulako. Indedi, oipa onse a padziko lapansi adzamwa nadzagugudiza nsenga zake. 9 Koma ine ndidzalalikira kosalekeza, ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wa Yakobo. 10 Ndipo ndidzatseteka nyanga zonse za oipa; koma nyanga za wolungama zidzakwezeka. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi