Kapena Yehova adzayang'anira chosayenerachi alikundichitira ine, ndipo Yehova adzandibwezera chabwino m'malo mwa kunditukwana kwa lero.
Masalimo 42:3 - Buku Lopatulika Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ntchito yanga ndi kulira usana ndi usiku, osalaŵa chakudya chilichonse. Ndipo anthu akhala akunena kuti, “Mulungu wako ali kuti?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Misozi yanga yakhala chakudya changa usana ndi usiku, pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti, “Mulungu wako ali kuti?” |
Kapena Yehova adzayang'anira chosayenerachi alikundichitira ine, ndipo Yehova adzandibwezera chabwino m'malo mwa kunditukwana kwa lero.
Adadzitengera kwa Yehova; kuti adzampulumutsa, amlanditse tsopano popeza akondwera naye.
Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga; pakunena ndine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?
Anenerenji amitundu, Ali kuti Mulungu wao? Kubwezera chilango cha mwazi wa atumiki anu umene anaukhetsa kudziwike pakati pa amitundu pamaso pathu.
Ndipo anansi athu amene anatonza Inu muwabwezere chotonza chao, kasanu ndi kawiri kumtima kwao, Ambuye.
Mbawanso inapeza nyumba, ndi namzeze chisa chake choikamo ana ake, pa maguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu, mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao?
Pamenepo mdani wanga adzachiona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu.
Pakuti ndaniyo, wa zamoyo zonse adamva mau a Mulungu wamoyo wakunena ali pakati pa moto, monga ife nakhala ndi moyo?