Masalimo 143 - Buku LopatulikaDavide apempha Mulungu amlanditse msanga kwa adani ake Salimo la Davide. 1 Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu. 2 Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu; pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense. 3 Pakuti mdani alondola moyo wanga; apondereza pansi moyo wanga; andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe. 4 Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine; mtima wanga utenga nkhawa m'kati mwanga. 5 Ndikumbukira masiku a kale lomwe; zija mudazichita ndilingirirapo; ndikamba pandekha za ntchito ya manja anu. 6 Nditambalitsira manja anga kwa Inu: Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula. 7 Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje. 8 Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu. 9 Mundilanditse kwa adani anga, Yehova; ndibisala mwa Inu. 10 Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha. 11 Mundipatse moyo, Yehova, chifukwa cha dzina lanu; mwa chilungamo chanu mutulutse moyo wanga m'sautso. 12 Ndipo mwa chifundo chanu mundidulire adani anga, ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga; pakuti ine ndine mtumiki wanu. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi