Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 143:1 - Buku Lopatulika

1 Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Imvani pemphero langa, Inu Chauta. Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga. Mundiyankhe chifukwa cha kukhulupirika kwanu ndi kulungama kwanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yehova imvani pemphero langa, mvetserani kulira kwanga kopempha chifundo; mwa kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu bwerani kudzandithandiza.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 143:1
8 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, mau amene munalankhula za mnyamata wanu ndi za nyumba yake, muwalimbikitse ku nthawi zonse nimuchite monga munalankhula.


Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga; munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.


Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga; tcherani khutu ku pemphero langa losatuluka m'milomo ya chinyengo.


Ndakhulupirira Inu, Yehova, ndikhale wopanda manyazi nthawi zonse, mwa chilungamo chanu ndipulumutseni ine.


Ndikwatuleni m'chilungamo chanu, ndi kundilanditsa, nditcherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa.


Ambuye, monga mwa chilungamo chanu chonse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zichoke kumzinda wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zochimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka chotonza cha onse otizungulira.


Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa