Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 79:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo anansi athu amene anatonza Inu muwabwezere chotonza chao, kasanu ndi kawiri kumtima kwao, Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo anansi athu amene anatonza Inu muwabwezere chotonza chao, kasanu ndi kawiri kumtima kwao, Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Inu Ambuye, kunyoza kuja kumene anthu a mitundu ina adakunyozani, muŵabwezere kasanunkaŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Mubwezere kwa anansi athu kasanu nʼkawiri kunyoza kumene ananyoza Inu Ambuye.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 79:12
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa iye, Chifukwa chake aliyense amene adzapha Kaini kudzabwezedwa kwa iye kasanu ndi kawiri. Ndipo Yehova anaika chizindikiro pa Kaini, kuti asamuphe aliyense akampeza.


Chifukwa cha mau a wotonza wochitira mwano; chifukwa cha mdani ndi wobwezera chilango.


Wotsutsanayo adzatonza kufikira liti, Mulungu? Kodi mdani adzanyoza dzina lanu nthawi yonse?


Wodalitsika Yehova kunthawi yonse. Amen ndi Amen.


koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri; idzapereka chuma chonse cha m'nyumba yake.


amene muchitira chifundo anthu zikwi; nimubwezera mphulupulu ya atate m'chifukwa cha ana ao a pambuyo pao, dzina lake ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu, Yehova wa makamu;


Ndipo udzadziwa kuti Ine Yehova ndidamva zamwano zako zonse udazinena pa mapiri a Israele, ndi kuti, Apasuka, apatsidwa kwa ife tiwadye.


chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndakweza dzanja langa Ine, ndi kuti, Zedi amitundu akuzungulira inu adzasenza manyazi ao.


Ndipo mukayenda motsutsana nane, osalola kumvera Ine; ndidzakuonjezerani miliri kasanu ndi kawiri, monga mwa zochimwa zanu.


Ine ndidzayenda nanu motsutsana mwa kukuzazirani, ndi kukulangani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.


Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa