Masalimo 11:2 - Buku Lopatulika Pakuti, onani, oipa akoka uta, apiringidza muvi wao pansinga, kuwaponyera mumdima oongoka mtima. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti, onani, oipa akoka uta, apiringidza muvi wao pansinga, kuwaponyera mumdima oongoka mtima. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Taonani, anthu oipa akunga uta ndipo akwinja muvi pa nsinga, kuti alase anthu a mtima wolungama. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti taona oyipa akunga mauta awo; ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta, pobisala pawo kuti alase olungama mtima. |
Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.
Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.
Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao; alikhe ozunzika ndi aumphawi, aphe amene ali oongoka m'njira.
Wolungama adzakondwera mwa Yehova, nadzakhulupirira Iye; ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza.
Akapanda kutembenuka munthu, iye adzanola lupanga lake; wakoka uta wake, naupiringidza.
Pakuti chiweruzo chidzabwera kunka kuchilungamo, ndipo oongoka mtima onse adzachitsata.
Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pachoonadi; pakuti alinkunkabe nachita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.
Nati Saulo, Ndidzampatsa iye, kuti amkhalire msampha, ndi kuti dzanja la Afilisti limgwere. Chifukwa chake Saulo ananena ndi Davide, Lero udzakhala mkamwini wanga kachiwiri.
Ndipo Davide anadziwa kuti Saulo analikulingalira zomchitira zoipa; nati kwa Abiyatara wansembe, Bwera kuno ndi efodi.