Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 142:3 - Buku Lopatulika

3 Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pamene mtima wanga ufooka, Inu mumadziŵa zoti ndichite. Adani anditchera msampha m'njira imene ndimayendamo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga, ndinu amene mudziwa njira yanga. Mʼnjira imene ndimayendamo anthu anditchera msampha mobisa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 142:3
20 Mawu Ofanana  

Koma adziwa njira ndilowayi; atandiyesa ndidzatuluka ngati golide.


Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama; koma mayendedwe a oipa adzatayika.


Yehova, imvani pemphero langa, ndipo mfuu wanga ufikire Inu.


Mtima wanga ukunga udzu womweta, nufota; popeza ndiiwala kudya mkate wanga.


Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.


Mundisunge ndisagwe mumsampha ananditcherawo, ndisakodwe m'makwekwe a iwo ochita zopanda pake.


Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine; mtima wanga utenga nkhawa m'kati mwanga.


Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku; mwandisuntha, simupeza kanthu; mwatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa.


Ndathiridwa pansi monga madzi, ndipo mafupa anga onse anaguluka. Mtima wanga ukunga sera; wasungunuka m'kati mwa matumbo anga.


Mundionjole mu ukonde umene ananditchera mobisika. Pakuti Inu ndinu mphamvu yanga.


Amemezana, alalira, atchereza mapazi anga, popeza alindira moyo wanga.


Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.


Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.


Ndikumbukira Mulungu ndipo ndivutika; ndilingalira ndipo mzimu wanga ukomoka.


Mfuu umvekedwe m'nyumba zao, pamene muwatengera khamu la nkhondo dzidzidzi; pakuti akumba dzenje lakundigwira ine, anabisira mapazi anga misampha.


Tauka, tafuula usiku, poyamba kulonda; tsanulira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye; takwezera maso ako kwa Iye, chifukwa cha moyo wa tiana tako, timene tilefuka ndi njala pa malekezero a makwalala onse.


Pomwepo Afarisi anamuka, nakhala upo wakumkola Iye m'kulankhula kwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa