Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 7:12 - Buku Lopatulika

12 Akapanda kutembenuka munthu, iye adzanola lupanga lake; wakoka uta wake, naupiringidza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Akapanda kutembenuka munthu, iye adzanola lupanga lake; wakoka uta wake, naupiringidza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ngati munthu salapa, Mulungu adzanola lupanga lake, adzakunga ndi kukoka uta wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ngati munthu satembenuka, Mulungu adzanola lupanga lake, Iye adzawerama ndi kukoka uta.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 7:12
15 Mawu Ofanana  

Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?


Yehova ndiye wolungama; anadulatu zingwe za oipa.


Mutibweze, Mulungu wa chipulumutso chathu, nimuletse udani wanu wa pa ife.


Mwadzudzula amitundu, mwaononga woipayo, mwafafaniza dzina lao kunthawi yonka muyaya.


Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalanga Leviyatani njoka yothamanga, ndi Leviyatani njoka yopindikapindika; nadzapha ching'ona chimene chili m'nyanja.


Pakuti lupanga langa lakhuta kumwamba; taonani, lidzatsikira pa Edomu, ndi pa anthu amene ndawatemberera, kuti aweruzidwe.


Chifukwa chake ndidzakuweruzani inu, nyumba ya Israele, yense monga mwa njira zake, ati Ambuye Yehova. Bwererani, nimutembenukire kuleka zolakwa zanu zonse, ndipo simudzakhumudwa nazo, ndi kuonongeka nayo mphulupulu.


Ndipo kudzakhala ngati kuombeza konyenga pamaso pa iwo amene anawalumbirira malumbiro; koma akumbutsa mphulupulu kuti akodwe.


Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele?


Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo: chifukwa chake mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto.


Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye;


ndikanola lupanga langa lonyezimira, ndi dzanja langa likagwira chiweruzo; ndidzabwezera chilango ondiukira, ndi kulanga ondida.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa