Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -

Masalimo 11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero


Salimo 11
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1 Mwa Yehova ine ndimathawiramo. Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti, “Thawira ku phiri lako ngati mbalame.

2 Pakuti taona oyipa akunga mauta awo; ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta, pobisala pawo kuti alase olungama mtima.

3 Tsono ngati maziko awonongeka, olungama angachite chiyani?”

4 Yehova ali mʼNyumba yake yoyera; Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba. Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu; maso ake amawayesa.

5 Yehova amayesa olungama, koma moyo wake umadana ndi oyipa, amene amakonda zachiwawa.

6 Iye adzakhuthulira pa oyipa makala amoto ndi sulufule woyaka; mphepo yotentha idzakhala yowayenera.

7 Pakuti Yehova ndi wolungama, Iye amakonda chilungamo; ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.

The Word of God in Contemporary Chichewa

Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®

Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®

Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Biblica, Inc.
Titsatireni:



Zotsatsa