Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 1:14 - Buku Lopatulika

Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pathambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pa thambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pambuyo pake Mulungu adati, “Kuthambo kukhale miyuni kuti izilekanitsa usana ndi usiku, ndiponso kuti ikhale zizindikiro za nyengo, masiku ndi zaka.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mulungu anati, “Pakhale zowunikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku. Ndipo zimenezi zikhale zizindikiro zoonetsa nyengo, masiku ndi zaka;

Onani mutuwo



Genesis 1:14
43 Mawu Ofanana  

Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachitatu.


Zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire padziko lapansi; ndipo kunatero.


Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.


ndiika utawaleza wanga m'mtambomo, ndipo udzakhala chizindikiro cha pangano lopangana ndi Ine ndi dziko lapansi.


Ngati awerengedwa makamu ake? Ndipo ndaniyo, kuunika kwake sikumtulukira?


Taonani, ngakhale mwezi ulibe kuwala; ndi nyenyezi siziyera pamaso pake;


Nyenyezi za chizirezire zide; uyembekezere kuunika, koma kuusowe; usaone kephenyuka kwa mbandakucha;


Kunena za maweruzo anu alimbikira kufikira lero; pakuti onsewa ndiwo atumiki anu.


Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi; mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira.


Anazikhazikanso kunthawi za nthawi; anazipatsa chilamulo chosatumphika.


Aleluya. Lemekezani Mulungu m'malo ake oyera; mlemekezeni m'thambo la mphamvu yake.


Ombani lipenga, pokhala mwezi, utakula mwezi, tsiku la phwando lathu.


Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lao ndi kuziwerenga; azitcha zonse maina ao, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.


Atero Yehova, Musaphunzire njira ya amitundu, musaope zizindikiro za m'thambo; pakuti amitundu aziopa izo.


Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ake agavira; Yehova wa makamu ndi dzina lake:


Pakuti Yehova atero: Ngati mukhoza kuswa pangano langa la usana ndi pangano langa la usiku, kuti usakhalenso usana ndi usiku, m'nyengo yao;


Yehova atero: Likaleka kukhala pangano langa la usana ndi usiku, ngati sindinalemba malemba a kumwamba ndi dziko lapansi;


Atero Ambuye Yehova, Pa chipata cha bwalo lam'kati choloza kum'mawa patsekedwe masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito; koma tsiku la Sabata patsegulidwe, ndi tsiku lokhala mwezi patsegulidwe.


Ndipo nsembe ya tsiku lokhala mwezi ikhale mwanawang'ombe wopanda chilema, ndi anaankhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zikhale zopanda chilema;


Dziko lapansi linjenjemera pamaso pao, thambo ligwedezeka, dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao;


Dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao.


Iye wakulenga Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, nasanduliza mdima wandiweyani ukhale m'mawa, nasanduliza usana ude ngati usiku, wakuitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova;


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Ambuye Yehova, ndidzalowetsa dzuwa usana, ndi kudetsa dziko pausana poyera.


nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.


Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:


Koma m'masikuwo, chitatha chisautso chimenecho, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzapatsa kuunika kwake,


Ndipo nsalu yotchinga ya mu Kachisi inang'ambika pakati.


ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse.


Ndipo ndinaona pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chimodzi, ndipo panali chivomezi chachikulu; ndi dzuwa lidada bii longa chiguduli cha ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi;


Ndipo mngelo wachinai anaomba lipenga, ndipo limodzi la magawo atatu a dzuwa linagwidwa, ndi limodzi la magawo atatu a mwezi, ndi limodzi la magawo atatu a nyenyezi; kuti limodzi la magawo ao atatu lidetsedwe, ndi kuti limodzi la magawo ake atatu a usana lisawale, ndi usiku momwemo.


Ndipo anatsegula pa chiphompho chakuya; ndipo unakwera utsi wotuluka m'chiphomphomo, ngati utsi wa ng'anjo yaikulu; ndipo dzuwa ndi thambo zinada, chifukwa cha utsiwo wa kuchiphomphocho.