Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 5:8 - Buku Lopatulika

8 Iye wakulenga Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, nasanduliza mdima wandiweyani ukhale m'mawa, nasanduliza usana ude ngati usiku, wakuitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Iye wakulenga Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, nasanduliza mdima wandiweyani ukhale m'mawa, nasanduliza usana ude ngati usiku, wakuitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira pa dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Iye uja ndiye amene adalenga nyenyezi za Akamwiniatsatana ndiponso Nsangwe, ndiye amene amasandutsa mdima kuti ukhale m'maŵa nasandutsa usana kuti ukhale usiku. Ndiye amene amaitana madzi am'nyanja ndi kuŵathira pa dziko lapansi. Dzina lake ndi Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 (Iye amene analenga nyenyezi za Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, amene amasandutsa mdima kuti ukhale mmawa ndi kudetsa usana kuti ukhale usiku, amene amayitana madzi a mʼnyanja ndi kuwathira pa dziko lapansi, Yehova ndiye dzina lake.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 5:8
23 Mawu Ofanana  

Avumbulutsa zozama mumdima, natulutsa mthunzi wa imfa ukhale poyera;


ngati aufikitsira dziko lake kulidzudzula, kapena kulichitira chifundo.


Kodi udziwa kukwezera mau ako kumitambo, kuti madzi ochuluka akukute?


Wolenga Mlalang'amba, Akamwiniatsatana, ndi Nsangwe, ndi Kumpotosimpita.


Muika mdima ndipo pali usiku; pamenepo zituluka zilombo zonse za m'thengo.


Anatumiza mdima ndipo kunada; ndipo sanapikisane nao mau ake.


Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa, m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzawasiya.


Tiyambasira khoma ngati wakhungu, inde tiyambasa monga iwo opanda maso; tiphunthwa usana monga m'chizirezire; tili m'malo amdima ngati akufa.


Chifukwa chake, taonani, ndidzadziwitsa iwo kamodzi aka, ndidzawadziwitsa dzanja langa ndi mphamvu yanga; ndipo adzadziwa kuti dzina langa ndine Yehova.


Atero Yehova wochita zake, Yehova wolenga zake kuti azikhazikitse; dzina lake ndi Yehova:


Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Ambuye Yehova, ndidzalowetsa dzuwa usana, ndi kudetsa dziko pausana poyera.


ndiye amene amanga zipinda zake zosanja m'mwamba, nakhazika tsindwi lake padziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lake ndiye Yehova.


anthu akukhala mumdima adaona kuwala kwakukulu, ndi kwa iwo okhala m'malo a mthunzi wa imfa, kuwala kunatulukira iwo.


Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa; kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa