Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 5:9 - Buku Lopatulika

9 wakufikitsa chionongeko pa wamphamvu modzidzimuka, kuti chionongekocho chigwere linga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 wakufikitsa chionongeko pa wamphamvu modzidzimuka, chionongeko nichigwera linga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndiyenso amene amakantha olamulira ankhanza, ndiye amene amagumula malinga ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Iyeyo amabweretsa chiwonongeko modzidzimutsa pa anthu amphamvu ndi kuwononga mizinda yotetezedwa),

Onani mutuwo Koperani




Amosi 5:9
7 Mawu Ofanana  

Nati, Tsegulani zenera la kum'mawa. Nalitsegula. Nati Elisa, Ponyani. Naponya. Nati iye, Muvi wa chipulumutso wa Yehova ndiwo muvi wa kukupulumutsani kwa Aaramu; popeza mudzakantha Aaramu mu Afeki mpaka mudzawatha.


Ndi Yehowasi mwana wa Yehowahazi analandanso m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele mizinda ija adailanda m'dzanja la Yehowahazi atate wake ndi nkhondo. Yehowasi anamkantha katatu, naibweza mizinda ya Israele.


Koma khamu la achilendo ako lidzafanana ndi fumbi losalala, ndi khamu la oopsa lidzakhala monga mungu wochokachoka; inde kudzaoneka modzidzimuka dzidzidzi.


Pakuti ngakhale mukadakantha nkhondo yonse ya Ababiloni akumenyana nanu, ngakhale akadatsala olasidwa okhaokha mwa iwo, koma iwowa akadauka yense m'hema wake ndi kutentha mzinda uwu ndi moto.


Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yake, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wake;


ndipo ndidzaononga mizinda ya m'dziko lako, ndi kupasula malinga ako onse;


nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa