Masalimo 150 - Buku LopatulikaZolengedwa zonse zilemekeze Mulungu 1 Aleluya. Lemekezani Mulungu m'malo ake oyera; mlemekezeni m'thambo la mphamvu yake. 2 Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunjinji. 3 Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze. 4 Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe: Mlemekezeni ndi zoimbira za zingwe ndi chitoliro. 5 Mlemekezeni ndi nsanje zomveka: Mlemekezeni ndi nsanje zoliritsa. 6 Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Aleluya. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi