Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 150:3 - Buku Lopatulika

3 Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Mtamandeni pomuimbira lipenga, mtamandeni ndi gitara ndi zeze.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mutamandeni poyimba malipenga, mutamandeni ndi pangwe ndi zeze.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 150:3
17 Mawu Ofanana  

Chomwecho Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anakwera nalo likasa la Yehova, ndi chimwemwe ndi kulira kwa malipenga.


Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoimbira za mitundumitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi maseche, ndi nsanje.


ndi Zekariya, ndi Aziyele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Uni, ndi Eliyabu, ndi Maaseiya, ndi Benaya, ndi zisakasa kuimbira mwa Alimoti;


Ndi Sebaniya, ndi Yosafati, ndi Netanele, ndi Amasai, ndi Zekariya, ndi Benaya, ndi Eliyezere, ansembe, analiza malipenga ku likasa la Mulungu; ndi Obededomu ndi Yehiya anali odikira a likasa.


Momwemo Aisraele onse anakwera nalo likasa la chipangano la Yehova ndi kufuula, ndi kumveka kwa lipenga, ndi mphalasa, ndi nsanje zomveketsa, ndi zisakasa, ndi azeze.


ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi malipenga ndi nsanje za iwo akumveketsadi, ndi zoimbira nyimbo za Mulungu; ndi ana a Yedutuni anakhala kuchipata.


Ndipo Davide ndi akazembe a gulu la nkhondo anapatulira utumikiwo ena a ana a Asafu, ndi a Hemani, ndi a Yedutuni, anenere ndi azeze, ndi zisakasa, ndi nsanje; ndi chiwerengo cha antchito monga mwa kutumikira kwao ndicho:


Ndipo anafika ku Yerusalemu ndi zisakasa, ndi azeze, ndi malipenga, kunyumba ya Yehova.


Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova;


Galamukani, chisakasa ndi zeze; ndidzauka ndekha mamawa.


Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe; amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.


Yamikani Yehova ndi zeze; muimbireni ndi chisakasa cha zingwe khumi.


Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa; pazeze ndi kulira kwake.


kuti pakumva inu mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, mugwadire ndi kulambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara;


Momwemo tsiku lakukondwera inu, ndi nyengo zoikidwa zanu, ndi poyamba miyezi yanu, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza, ndi pa nsembe zanu zoyamika; ndipo akhale kwa inu chikumbutso pamaso pa Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa