Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 24:29 - Buku Lopatulika

29 Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 “Akadzangotha mavuto a masiku amenewo, dzuŵa lidzada, mwezi udzaleka kuŵala, nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo, ndipo mphamvu zamumlengalenga zidzagwedezeka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 “Akadzangotha mavuto a masiku amenewo, “ ‘dzuwa lidzadetsedwa, ndipo mwezi sudzawala; nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu za mmwamba zidzagwedezeka.’

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 24:29
21 Mawu Ofanana  

ngakhale lisanade dzuwa, ndi kuunika, ndi mwezi, ndi nyenyezi, mitambo ndi kubweranso italeka mvula;


Chifukwa nyenyezi za kumwamba ndi makamu ao sizidzawala; dzuwa lidzada m'kutuluka kwake, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.


Pompo mwezi udzanyazitsidwa, ndi dzuwa lidzakhala ndi manyazi, pakuti Yehova wa makamu adzalamulira chaulemerero m'phiri la Ziyoni, ndi mu Yerusalemu, ndi pamaso pa akuluakulu ake.


Ndipo makamu onse a kumwamba adzasungunuka, ndi miyamba idzapindika pamodzi ngati mpukutu; makamu ao onse adzafota monga tsamba limafota pampesa ndi kugwa, ndi monga tsamba lifota pamkuyu.


Dziko lapansi linjenjemera pamaso pao, thambo ligwedezeka, dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao;


Dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao.


Kodi tsiku la Yehova silidzakhala la mdima, si la kuunika ai? Lakuda bii, lopanda kuwala m'menemo?


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Ambuye Yehova, ndidzalowetsa dzuwa usana, ndi kudetsa dziko pausana poyera.


pakuti pomwepo padzakhala masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.


Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.


Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m'mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa.


Ndipo mngelo wachinai anaomba lipenga, ndipo limodzi la magawo atatu a dzuwa linagwidwa, ndi limodzi la magawo atatu a mwezi, ndi limodzi la magawo atatu a nyenyezi; kuti limodzi la magawo ao atatu lidetsedwe, ndi kuti limodzi la magawo ake atatu a usana lisawale, ndi usiku momwemo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa