Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 24:28 - Buku Lopatulika

28 Kumene kulikonse kuli mtembo, miimba idzasonkhanira konko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Kumene kulikonse uli mtembo, miimba idzasonkhanira konko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 “Paja adati, Kulikonse kumene kwafera chinthu, miphamba imasonkhana kumeneko.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Kulikonse kuli chinthu cha kufa, makwangwala adzasonkhanako.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 24:28
7 Mawu Ofanana  

Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pake ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe.


Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova, Nena kwa mbalame za mitundu yonse, ndi kwa nyama zonse zakuthengo, Memezanani, idzani, sonkhanani kumbali zonse, kudza kunsembe yanga imene ndikupherani, ndiyo nsembe yaikulu pa mapiri a Israele, kuti mudzadye nyama ndi kumwa mwazi.


Akavalo ao aposa anyalugwe liwiro lao, aposa mimbulu ya madzulo ukali wao, ndipo apakavalo ao atanda; inde apakavalo ao afumira kutali; auluka ngati chiombankhanga chofulumira kudya.


Ndipo anayankha nanena kwa Iye, Kuti, Ambuye? Ndipo anati kwa iwo, Pamene pali mtembo, pomweponso miimba idzasonkhanidwa.


Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamve malankhulidwe ao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa