Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 24:30 - Buku Lopatulika

30 ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo chizindikiro cha Mwana wa Munthu; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa Munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo chizindikiro cha Mwana wa Munthu; ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa Munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Pamenepo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka ku thambo. Anthu a mitundu yonse ya pansi pano adzayamba kulira, ndipo adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 “Pa nthawi imeneyo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka mlengalenga, ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalira. Idzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 24:30
17 Mawu Ofanana  

Ndinaona m'masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pake.


Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.


Tsiku lomwelo kudzakhala maliro aakulu mu Yerusalemu, ngati maliro a Hadadirimoni m'chigwa cha Megido.


Ndipo pamene Iye analikukhala pansi paphiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?


Ndipo monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.


ndipo iwo sanadziwe kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.


Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu ali kukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.


Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa Munthu alinkudza m'mitambo ndi mphamvu yaikulu, ndi ulemerero.


Tiuzeni, zinthu izi zidzachitika liti? Ndi chotani chizindikiro chake chakuti zili pafupi pa kumalizidwa zinthu izi zonse?


Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa Munthu alinkudza mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.


Koma kuyambira tsopano Mwana wa Munthu adzakhala padzanja lamanja la mphamvu ya Mulungu.


amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.


ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake,


Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso lililonse lidzampenya Iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a padziko adzamlira Iye. Terotu. Amen.


Ndipo chizindikiro chachikulu chinaoneka m'mwamba; mkazi wovekedwa dzuwa, ndi mwezi kumapazi ake, ndi pamutu pake korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa