Chivumbulutso 8 - Buku LopatulikaAtsegula chosindikiza chachisanu ndi chiwiri. Angelo asanu ndi awiri, ndi malipenga oyamba anai 1 Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chiwiri, munali chete mu Mwamba monga mwa nthawi ya ora latheka. 2 Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri. 3 Ndipo anadza mngelo wina, naima paguwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolide; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse paguwa la nsembe lagolide, lokhala kumpando wachifumu. 4 Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kutuluka m'dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu. 5 Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi moto wopala paguwa la nsembe, nauponya padziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi chivomezi. 6 Ndipo angelo asanu ndi awiri akukhala nao malipenga anadzikonzera kuti aombe. 7 Ndipo woyamba anaomba lipenga, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosakaniza ndi mwazi, ndipo anazitaya padziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera. 8 Ndipo mngelo wachiwiri anaomba lipenga, ndipo monga ngati phiri lalikulu lakupserera ndi moto linaponyedwa m'nyanja; ndipo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka mwazi; 9 ndipo lidafa limodzi la magawo atatu a zolengedwa zili m'nyanja, zokhala ndi moyo; ndipo limodzi la magawo atatu a zombo lidaonongeka. 10 Ndipo mngelo wachitatu anaomba lipenga, ndipo idagwa kuchokera kumwamba nyenyezi yaikulu, yoyaka ngati muuni, ndipo idagwa pa limodzi la magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe amadzi; 11 ndipo dzina lake la nyenyeziwo alitcha Chowawa; ndipo limodzi la magawo atatu a madzi lidasanduka chowawa; ndipo anthu ambiri adafa pakumwa madzi, pakuti asananduka owawa. 12 Ndipo mngelo wachinai anaomba lipenga, ndipo limodzi la magawo atatu a dzuwa linagwidwa, ndi limodzi la magawo atatu a mwezi, ndi limodzi la magawo atatu a nyenyezi; kuti limodzi la magawo ao atatu lidetsedwe, ndi kuti limodzi la magawo ake atatu a usana lisawale, ndi usiku momwemo. 13 Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva chiombankhanga chilikuuluka pakati pamwamba, ndi kunena ndi mau aakulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi