Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, kuti zinthu zotisokoneza maganizo cholinga chake chachikulu ndi kutisokoneza pa chifuniro cha Mulungu. Zimatipangitsa kuchita zinthu zopanda phindu pa moyo wathu komanso kukula kwathu mwauzimu.
Muyu ndiye amapezerapo mwayi tikamafooka, tikasamala kwambiri mawu a Mulungu komanso tikapadzira pemphero. Ndikofunika kudziwa zomwe zikutisokoneza ndikupempha Mulungu kuti atipatse mpungu kuti tigonjetse chilichonse choletsa kukula kwathu.
Malemba amatiuza mu Afilipi 4:13 kuti, “Ndingathe kuchita zonse mwa Iye wondichititsa mphamvu”. Chifukwa chake, khulupirirani kuti Yesu adzakupatsani njira yothawa ndikukuthandizani kugonjetsera chilichonse chimene chikukusokonezani.
Ndinu olimba mtima. Musalole kuti chilichonse chikulamulireni. Dziperekeni kwa Khristu, mufuneni ndi mtima wanu wonse ndipo adzagwira ntchito mwamphamvu mwa inu.
Koma ichi ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakutchereni msampha, koma kukuthandizani kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye, opanda chocheukitsa.
Musakonde dziko lapansi, kapena za m'dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye. Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.
Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.
Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi. Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.
Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.
Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. koma mudzikundikire nokha chuma mu Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.
koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.
Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.
Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.
Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho.
Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawirikawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Khristu; chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko. Penyererani agalu, penyererani ochita zoipa, penyererani choduladula; Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu;
Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda chipatso.
Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.
Ndipo zija zinagwa kumingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.
pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalamatiya.
Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;
Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;
Maso ako ayang'ane m'tsogolo, zikope zako zipenye moongoka. Sinkhasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako; njira zako zonse zikonzeke. Usapatuke kudzanja lamanja kapena kulamanzere; suntha phazi lako kusiya zoipa.
Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.
Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.
ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:
Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake. Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo. Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka; ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe. Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye: ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao; kuti pangakhale wachigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nao mtanda umodzi wa chakudya. Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeze malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi. Pakuti simunayandikire phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe, ndi mau a lipenga, ndi manenedwe a mau, manenedwe amene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau; Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Khristu, akondwanso nazo, nagonjetsedwa, zotsiriza zao zidzaipa koposa zoyambazo.
Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba.
Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira.
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu;
Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa nacho chimodzi.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.
Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi.
Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.
popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.
Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.
koma ndiona lamulo lina m'ziwalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la uchimo m'ziwalo zanga.
komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo;
Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero.
Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali.
nasankhula kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthawi;
Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa kusaweruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazilala.
Koma Yesu anati kwa iye, Palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang'ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.
ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.
Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.
kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi.
mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi aakulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wake, mutapulumuka kuchivundi chili padziko lapansi m'chilakolako.
woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.
Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera.
Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
Chotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.
Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani; ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse; pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi. Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika. Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe. Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani. Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu, ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.
tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine. Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzautaya: koma iye amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza. Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?
Usadzitopetse kuti ulemere; leka nzeru yakoyako. Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.
Ndili ndi yani Kumwamba, koma Inu? Ndipo padziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu. Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.
ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani; kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu.
Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu. Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.
Ndipo iye amene satenga mtanda wake, natsata pambuyo panga, sayenera Ine. Iye amene apeza moyo wake, adzautaya; ndi iye amene ataya moyo wake, chifukwa cha Ine, adzaupeza.
Kodi simudziwa kuti iwo akuchita makani a liwiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire. Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda. Chifukwa chake ine ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, si monga ngati kupanda mlengalenga; koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.
Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munaipambana; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;
ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;
Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.
Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse mu Gehena. Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losamuka thupi lako lonse ku Gehena.
Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,
Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.
Chifukwa chake tisaweruzanenso wina mnzake; koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asaike chokhumudwitsa panjira ya mbale wake, kapena chomphunthwitsa.
kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,
Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.
Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo; koma opabe Yehova tsiku lonse. Pakutitu padzakhala mphotho; ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.
Usiku wapita, ndi mbandakucha wayandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ndipo tivale zida za kuunika.
Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse; ndisasokere kusiyana nao malamulo anu. Ndizindikira koposa okalamba popeza ndinasunga malangizo anu. Ndinaletsa mapazi anga njira iliyonse yaoipa, kuti ndisamalire mau anu. Sindinapatukane nao maweruzo anu; pakuti Inu munandiphunzitsa. Mau anu azunadi powalawa ine! Koposa uchi m'kamwa mwanga. Malangizo anu andizindikiritsa; chifukwa chake ndidana nao mayendedwe onse achinyengo. Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga. Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama. Ndazunzika kwambiri: Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu. Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga, ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu. Moyo wanga ukhala m'dzanja langa chikhalire; koma sindiiwala chilamulo chanu. Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.
Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake. Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi;
Koma iwo a Khristu Yesu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake. Ngati tili ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende.
koma nkhani zachabe ndi za akazi okalamba ukane. Ndipo udzizoloweretse kuchita chipembedzo; pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang'ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kucha. Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi. Adzawapereka kumphamvu ya lupanga; iwo adzakhala gawo la ankhandwe. Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu; yense wakulumbirira iye adzatamandira; pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa. Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu, monga ndinakuonani m'malo oyera. Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani.
Koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga kuchiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro; kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.
Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo, ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.
Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.
Pakuti mau a mtanda ali ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tilikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.
Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.
Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.
Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.
Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m'mantha anga onse. Iwo anayang'ana Iye nasanguluka; ndipo pankhope pao sipadzachita manyazi.
ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni, kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wake wa Iye yekha, ndi ulemerero.
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.
kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;
kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu, kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'chikondi,