Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Aefeso 6:16 - Buku Lopatulika

16 koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Kuwonjezera pa zonsezi, nyamulani chishango cha chikhulupiriro, ndipo ndi chimenechi mudzatha kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya oyipayo.

Onani mutuwo Koperani




Aefeso 6:16
16 Mawu Ofanana  

Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.


Ndiponso munandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa.


Mivi yakuthwa ya chiphona, ndi makala tsanya.


Ndipo anamkonzera zida za imfa; mivi yake aipanga ikhale yansakali.


Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.


Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo choonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo.


Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.


Koma ife popeza tili a usana tisaledzere, titavala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa