Masalimo 135 - Buku LopatulikaMulungu alemekezedwa pa ukulu wake. Mafano ndi achabe 1 Aleluya; Lemekezani dzina la Yehova! Lemekezani inu atumiki a Yehova. 2 Inu akuimirira m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu. 3 Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino; muimbire zolemekeza dzina lake; pakuti nkokondweretsa kutero. 4 Pakuti Yehova anadzisankhira Yakobo, Israele, akhale chuma chake chenicheni. 5 Pakuti ndidziwa kuti Yehova ndi wamkulu, ndi Ambuye wathu aposa milungu yonse. 6 Chilichonse chimkonda Yehova achichita, kumwamba ndi padziko lapansi, m'nyanja ndi mozama monse. 7 Akweza mitambo ichokere ku malekezero a dziko lapansi; ang'animitsa mphezi zidzetse mvula; atulutsa mphepo mosungira mwake. 8 Anapanda oyamba a Ejipito, kuyambira munthu kufikira zoweta. 9 Anatumiza zizindikiro ndi zodabwitsa pakati pako, Ejipito iwe, pa Farao ndi pa omtumikira onse. 10 Ndiye amene anapanda amitundu ambiri, napha mafumu amphamvu; 11 Sihoni mfumu ya Aamori, ndi Ogi mfumu ya Basani, ndi maufumu onse a Kanani: 12 Ndipo anapereka dziko lao likhale cholowa, cholowa cha kwa Israele anthu ake. 13 Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha; chikumbukiro chanu, Yehova, kufikira mibadwomibadwo. 14 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake, koma adzaleka atumiki ake. 15 Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golide, ntchito ya manja a anthu. 16 Pakamwa ali napo koma osalankhula; maso ali nao, koma osapenya; 17 makutu ali nao, koma osamva; inde, pakamwa pao palibe mpweya. 18 Akuwapanga adzafanana nao; inde, onse akuwakhulupirira. 19 A nyumba ya Israele inu, lemekezani Yehova: A nyumba ya Aroni inu, lemekezani Yehova: 20 A nyumba ya Levi inu, lemekezani Yehova: Inu akuopa Yehova, lemekezani Yehova. 21 Alemekezedwe Yehova kuchokera mu Ziyoni, amene akhala mu Yerusalemu. Aleluya. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi