Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 135:14 - Buku Lopatulika

14 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake, koma adzaleka atumiki ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake, koma adzaleka atumiki ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Pakuti Chauta adzaweruza anthu ake kuti alibe mlandu, adzachitira chifundo atumiki ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Pakuti Yehova adzaonetsa kuti anthu ake ngosalakwa, ndipo adzachitira chifundo atumiki ake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 135:14
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anatuma mthenga ku Yerusalemu kuuononga; ndipo poti auononge, Yehova anapenya, naleka choipachi; nati kwa mthenga wakuononga, Chakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndi mthenga wa Yehova anaima pa dwale la Orinani Myebusi.


Kumwamba adzaitana zakumwamba, ndi dziko lapansi, kuti aweruze anthu ake.


Yehova aweruza anthu mlandu; mundiweruze, Yehova, monga mwa chilungamo changa, ndi ungwiro wanga uli mwa ine.


Bwerani, Yehova; kufikira liti? Ndipo alekeni atumiki anu.


Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi.


Ndipo Yehova anachileka. Sichidzachitika, ati Yehova.


Ndipo Yehova anachileka. Ichi chomwe sichidzachitika, ati Ambuye Yehova.


Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho.


Popeza Yehova adzaweruza anthu ake, nadzachitira nsoni anthu ake; pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha, wosatsala womangika kapena waufulu.


Pamenepo anachotsa milungu yachilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wake unagwidwa chisoni chifukwa cha mavuto a Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa