Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 135:5 - Buku Lopatulika

5 Pakuti ndidziwa kuti Yehova ndi wamkulu, ndi Ambuye wathu aposa milungu yonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pakuti ndidziwa kuti Yehova ndi wamkulu, ndi Ambuye wathu aposa milungu yonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Pakuti ndimadziŵa kuti Chauta ndi wamkulu, kuti Chauta, Mulungu wathu, ndi wamphamvu kupambana milungu yonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndikudziwa kuti Yehova ndi wamkulu, kuti Ambuye athu ndi wamkulu kuposa milungu yonse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 135:5
13 Mawu Ofanana  

Ambuye wathu ndi wamkulu ndi wa mphamvu zambiri; nzeru yake njosatha.


Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.


Pakuti kuli yani kuthambo timlinganize ndi Yehova? Afanana ndi Yehova ndani mwa ana a amphamvu?


Pakuti Yehova ndiye Mulungu wamkulu; ndi mfumu yaikulu yoposa milungu yonse.


Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi, ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu ina yonse.


Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati chinsalu, naliyala monga hema wakukhalamo;


Mudzandifanizira Ine ndi yani tsono, kuti ndilingane naye, ati Woyerayo.


Chifukwa chake ndilamulira kuti anthu ali onse, mtundu uliwonse, ndi a manenedwe ali onse, akunenera molakwira Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, adzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zao zidzasanduka dzala; popeza palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.


Popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa ambuye; Mulungu wamkulu, wamphamvu, ndi woopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira chokometsera mlandu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa