Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 135:6 - Buku Lopatulika

6 Chilichonse chimkonda Yehova achichita, kumwamba ndi padziko lapansi, m'nyanja ndi mozama monse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Chilichonse chimkonda Yehova achichita, kumwamba ndi pa dziko lapansi, m'nyanja ndi mozama monse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Chilichonse chimene Chauta amafuna kuchita amachitadi kumwamba ndi pa dziko lapansi, m'nyanja ndi monse mozama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera, kumwamba ndi dziko lapansi, ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 135:6
13 Mawu Ofanana  

Ndidziwa kuti mukhoza kuchita zonse, ndi kuti palibe choletsa cholingirira chanu chilichonse.


Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba; achita chilichonse chimkonda.


Chiweruzo cha Yehova chikhazikika chikhazikikire, zolingirira za m'mtima mwake ku mibadwomibadwo.


Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa; analamulira, ndipo chinakhazikika.


ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse;


Nadzakuinga kukuchotsa kwa anthu, ndi pokhala pako udzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; adzakudyetsa udzu ngati ng'ombe; ndipo zidzakupitira nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka udzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.


ndi okhala padziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala padziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?


Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.


ndiye amene amanga zipinda zake zosanja m'mwamba, nakhazika tsindwi lake padziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lake ndiye Yehova.


Ndipo pa ulonda wachinai wa usiku, Iye anadza kwa iwo, nayenda pamwamba pa nyanja.


Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa