Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 135:9 - Buku Lopatulika

9 Anatumiza zizindikiro ndi zodabwitsa pakati pako, Ejipito iwe, pa Farao ndi pa omtumikira onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Anatumiza zizindikiro ndi zodabwitsa pakati pako, Ejipito iwe, pa Farao ndi pa omtumikira onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 amene adaonetsa Farao ndi atumiki ake onse zizindikiro zamphamvu ndi zodabwitsa m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Iye anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa pakati pako, iwe Igupto, kutsutsana ndi Farao pamodzi ndi atumiki ake onse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 135:9
11 Mawu Ofanana  

nimunachitira zizindikiro ndi zodabwitsa Farao ndi akapolo ake onse, ndi anthu onse a m'dziko lake; popeza munadziwa kuti anawachitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino.


Nakhuthula Farao ndi khamu lake mu Nyanja Yofiira: pakuti chifundo chake nchosatha.


Anachita chodabwitsa pamaso pa makolo ao, m'dziko la Ejipito kuchidikha cha Zowani.


Ameneyo anawatsogolera, natuluka nao atachita zozizwa ndi zizindikiro mu Ejipito, ndi mu Nyanja Yofiira, ndi m'chipululu zaka makumi anai.


Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?


Ndipo Yehova anapatsa zizindikiro ndi zozizwa zazikulu ndi zowawa mu Ejipito, pa Farao, ndi pa nyumba yake yonse, pamaso pathu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa