Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 135:21 - Buku Lopatulika

21 Alemekezedwe Yehova kuchokera mu Ziyoni, amene akhala mu Yerusalemu. Aleluya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Alemekezedwe Yehova kuchokera m'Ziyoni, amene akhala m'Yerusalemu. Aleluya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Atamandike ku Ziyoni Chauta, amene amakhala ku Yerusalemu! Tamandani Chauta!

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Wodalitsika ndi Yehova kuchokera mʼZiyoni, amene amakhala mu Yerusalemu. Tamandani Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 135:21
13 Mawu Ofanana  

Pakuti Davide anati, Yehova Mulungu wa Israele wapumulitsa anthu ake; ndipo akhala mu Yerusalemu kosatha;


Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.


pamodzi ndi siliva ndi golide zilizonse ukazipeza m'dziko lonse la ku Babiloni, pamodzi ndi chopereka chaufulu cha anthu, ndi cha ansembe, akuperekera mwaufulu nyumba ya Mulungu wao ili ku Yerusalemu;


Yehova adzakudalitsa ali mu Ziyoni; ndipo udzaona zokoma za Yerusalemu masiku onse a moyo wako.


Yehova, ali mu Ziyoni, akudalitseni; ndiye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi.


Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.


Phiri la Ziyoni, chikhalidwe chake nchokoma kumbali zake za kumpoto, ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi, mzinda wa mfumu yaikulu.


Mulungu adziwika m'zinyumba zake ngati msanje.


Tidalingalira zachifundo chanu, Mulungu, m'kati mwa Kachisi wanu.


Msasa wake unali mu Salemu, ndipo pokhala Iye mu Ziyoni.


Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.


Sayang'anira mphulupulu ili mu Yakobo, kapena sapenya kupulukira kuli mu Israele. Yehova Mulungu wake ali ndi iye, ndi mfuu wa mfumu uli pakati pao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa