Numeri 23:7 - Buku Lopatulika Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ku Aramu ananditenga Balaki, mfumu ya Mowabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa, Idza, udzanditembererere Yakobo. Idza, nudzanyoze Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ku Aramu ananditenga Balaki, mfumu ya Mowabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa, Idza, udzanditembererere Yakobo. Idza, nudzanyoze Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Balamu adayamba kulankhula mau auneneri, adati, “Balaki mfumu ya ku Mowabu yandiitana kuchokera ku Aramu, ku mapiri akuvuma, kuti, ‘Bwerani, dzatemberereni Yakobe m'malo mwanga, bwerani mudzamfunire Israele zoipa.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Balaamu ananena uthenga wake: “Balaki ananditenga kuchoka ku Aramu, mfumu ya ku Mowabu kuchokera ku mapiri a kummawa. Iye anati, ‘Bwera, temberera Yakobo mʼmalo mwanga, pita nyoza Israeli.’ |
Tauka, nupite ku Padanaramu, kunyumba ya Betuele, atate wa amai ako; ukadzitengere mkazi wa kumeneko kwa ana aakazi a Labani mlongo wake wa amai ako.
Ndipo wotsatana naye Eleazara mwana wa Dodo mwana wa Mwahohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atachoka Aisraele;
Monga mpheta ilikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka, momwemo temberero la pachabe silifikira.
Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! Andichotsera ili! Agawira opikisana minda yathu.
Kodi sadzamnenera fanizo onsewo, ndi mwambi womnyodola, ndi kuti, Tsoka iye wochulukitsa zimene sizili zake? Mpaka liti? Iye wodzisenzera zigwiriro.
Taonani, anthu awa adatuluka mu Ejipito aphimba nkhope ya dziko, idzatu unditembererere awa; kapena ndidzakhoza kulimbana nao nkhondo, ndi kuwapirikitsa.
popeza ndidzakuchitira ulemu waukulu, ndipo zonse unena ndi ine ndidzachita; chifukwa chake idzatu, unditembererere anthu awa.
Ndipo anabwerera kwa iye, ndipo, taonani, analikuima pa nsembe yopsereza yake, iye ndi akalonga onse a Mowabu.
Ndipo ananena fanizo lake, nati, Balamu mwana wa Beori anenetsa, ndi munthu wotsinzina masoyo anenetsa;
Ndipo anayang'ana Akeni, nanena fanizo lake, nati, kwanu nkokhazikika, wamanga chisa chako m'thanthwe.
Pamenepo ananena fanizo lake, nati, Balamu mwana wa Beori anenetsa, ndi munthuyo anatsinzina maso anenetsa;
Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anachitenga, nachibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.
kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri, kuti, Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo; ndidzawulula zinthu zobisika chiyambire kukhazikidwa kwake kwa dziko lapansi.
Ndipo anayesa kumgwira Iye; koma anaopa khamu la anthu, pakuti anazindikira kuti Iye anakamba fanizo ili kuwatsutsa iwo; ndipo anamsiya Iye, nachoka.
popeza sanakumane nanu ndi mkate ndi madzi m'njira muja munatuluka mu Ejipito; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesopotamiya, kuti akutemberereni.
Nati Mfilistiyo, Ine ndinyoza makamu a nkhondo a Israele lero; mundipatse munthu, kuti tilimbane ife awiri.
Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi chimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.
Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israele amene iwe unawanyoza.