Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 17:45 - Buku Lopatulika

45 Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israele amene iwe unawanyoza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

45 Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israele amene iwe unawanyoza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

45 Koma Davide adauza Mfilistiyo kuti, “Wadza kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo. Koma ine ndikudza kwa iwe m'dzina la Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa magulu ankhondo a Aisraele, amene iwe wamunyoza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

45 Koma Davide anati kwa Mfilisitiyo, “Iwe wabwera kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo, koma ine ndikubwera kwa iwe mʼdzina la Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa ankhondo Aisraeli amene iwe ukuwanyoza.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 17:45
21 Mawu Ofanana  

Natuluka Asa pamaso pake, nanika nkhondoyi m'chigwa cha Zefati ku Maresa.


pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo. Ndipo anthu anachirikizika ndi mau a Hezekiya mfumu ya Yuda.


Thandizo lathu lili m'dzina la Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.


Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.


Iwowa anagonjeka, nagwa; koma ife tauka, ndipo takhala chilili.


Chipulumutso ncha Yehova; dalitso lanu likhale pa anthu anu.


Pakuti uta wanga, ndipo lupanga langa silingandipulumutse.


Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.


Ndani amene, iwe wamtonza ndi kumlalatira? Ndani amene iwe wakwezera mau ako ndi kutukulira maso ako kumwamba? Ndiye Woyera wa Israele.


Koma ndidziwa pokhala pansi pako, ndi kutuluka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundikwiyira kwako.


(pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga);


si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu;


Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.


Nati Mfilistiyo, Ine ndinyoza makamu a nkhondo a Israele lero; mundipatse munthu, kuti tilimbane ife awiri.


Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamchitira chiyani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kuchotsa tonzo lake pakati pa Israele? Pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?


Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi chimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.


nakuta msongolo wake ndi chovala chamkuwa, ndiponso pachikota pake panali nthungo yamkuwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa