1 Samueli 17:46 - Buku Lopatulika46 Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201446 Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa46 Lero lomwe lino Chauta akupereka m'manja mwanga. Ndikulasa ndi kukugwetsa pansi, ndipo ndikudula mutu. Mitembo ya magulu ankhondo a Afilisti ndiipereka lero lino kwa mbalame zamumlengalenga, ndi kwa zilombo zakuthengo, kuti dziko lonse lapansi lidziŵe kuti kuli Mulungu ku dziko la Israele. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero46 Anatinso lero lino Yehova adzakupereka mʼmanja mwanga. Ndidzakukantha ndi kudula mutu wako. Ndidzapereka mitembo ya asilikali a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo zakuthengo ndipo dziko lonse lapansi lidzadziwa kuti mu Israeli muli Mulungu. Onani mutuwo |