Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 17:44 - Buku Lopatulika

44 Ndipo Mfilistiyo anati kwa Davide, Idza kuno kwa ine, ndidzapatsa mnofu wako kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo zakuthengo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Ndipo Mfilistiyo anati kwa Davide, Idza kuno kwa ine, ndidzapatsa mnofu wako kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za kuthengo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 Kenaka adauza Davide kuti, “Idza kuno, mnofu wako ndidyetsera mbalame zamumlengalenga ndi zilombo zakuthengo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 Iye anatinso, “Bwera kuno ndipo ndidzapereka mnofu wako kwa mbalame zamlengalenga ndi kwa zirombo zakuthengo!”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 17:44
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Rizipa mwana wamkazi wa Aya anatenga chiguduli, nadziyalira ichi pathanthwe, kuyambira pakukolola kufikira madzi ochokera kumwamba adawagwera; ndipo sadalole mbalame za m'mlengalenga kutera pa iwo usana, kapena zilombo zakuthengo usiku.


Mtima wa munthu unyada asanaonongeke; koma chifatso chitsogolera ulemu.


ndidzapereka iwo m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la iwo akufuna moyo wao; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za mlengalenga, ndi cha zilombo za padziko lapansi.


Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m'chuma chake;


Wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa kalonga wa Tiro, Atero Ambuye Yehova, Popeza mtima wako wadzikweza, nuti, Ine ndine Mulungu, ndikhala pa mpando wa Mulungu pakati pa nyanja, ungakhale uli munthu, wosati Mulungu, ungakhale waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu,


Ndipo ndinaona mngelo alikuima m'dzuwa; ndipo anafuula ndi mau aakulu akunena ndi mbalame zonse zakuuluka pakati pa mlengalenga: Idzani kuno, sonkhanani kuphwando la Mulungu wamkulu,


Ndipo a ku kabomawo anayankha Yonatani ndi wonyamula zida zake, nati, Kwerani kuno kwa ife, tikuonetseni kanthu. Ndipo Yonatani, anauza wonyamula zida zake, Kwera unditsate m'mbuyo, pakuti Yehova wawapereka m'dzanja la Israele.


Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa