Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 12:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo anayesa kumgwira Iye; koma anaopa khamu la anthu, pakuti anazindikira kuti Iye anakamba fanizo ili kuwatsutsa iwo; ndipo anamsiya Iye, nachoka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo anayesa kumgwira Iye; koma anaopa khamu la anthu, pakuti anazindikira kuti Iye anakamba fanizo ili kuwatsutsa iwo; ndipo anamsiya Iye, nachoka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Pamene akulu a Ayuda aja adazindikira kuti fanizolo Yesu ankaphera iwowo, adafunitsitsa kumugwira, koma ankaopa khamu la anthu. Tsono adangomusiya nachokapo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ndipo akulu a ansembe, aphunzitsi a malamulo ndi akuluakulu anafunafuna njira yoti amugwirire Iye chifukwa amadziwa kuti anayankhula fanizoli mowatsutsa iwo. Koma amaopa gulu la anthu; ndipo anamusiya napita.

Onani mutuwo Koperani




Marko 12:12
13 Mawu Ofanana  

Koma tikati, Kwa anthu, tiopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri.


Ndipo pamene iwo anamva, anazizwa, namsiya Iye, nachokapo.


Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, chifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.


Koma tikati, Kwa anthu, anaopa anthuwo; pakuti onse anamuyesa Yohane mneneri ndithu.


Ndipo alembi ndi ansembe aakulu anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili.


Ndiponso, tikanena, Uchokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri.


Pamenepo ena a iwo a ku Yerusalemu ananena, Kodi suyu amene afuna kumupha?


Pamenepo anafuna kumgwira Iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake siinafike.


Koma ena mwa iwo anafuna kumgwira Iye; koma palibe munthu anamgwira kumanja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa