Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 28:7 - Buku Lopatulika

7 ndiponso kuti Yakobo anamvera atate wake ndi amake, nanka ku Padanaramu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 ndiponso kuti Yakobo anamvera atate wake ndi amake, nanka ku Padanaramu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Adamva kuti Yakobe wamvera bambo wake ndi mai wake, ndipo kuti wapita ku Mesopotamiya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Yakobo anamvera abambo ake ndi amayi ake ndi kupita ku Padanaramu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 28:7
11 Mawu Ofanana  

ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.


Ndipo tsopano mwana wanga, tamvera mau anga: tauka, nuthawire kwa Labani mlongo wanga ku Harani;


Ndipo anaona Esau kuti Isaki anamdalitsa Yakobo namtumiza ku Padanaramu kuti atenge mkazi wa kumeneko; ndiponso kuti pamene anamdalitsa iye, anamuuza iye kuti, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani;


ndipo Esau anaona kuti ana aakazi a Kanani sanakondweretse Isaki atate wake:


Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.


Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amai ako;


Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makwangwala a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.


Aliyense aope mai wake, ndi atate wake; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino.


kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.


Ana inu, mverani akubala inu m'zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa