Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Miyambo 26:2 - Buku Lopatulika

2 Monga mpheta ilikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka, momwemo temberero la pachabe silifikira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Monga mpheta ilikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka, momwemo temberero la pachabe silifikira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Monga imachitira mpheta yokhalira kuuluka, monga amachitira namzeze kumangoti zwezwezwe, ndimonso limachitira temberero lopanda chifukwa, silitha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ngati timba wokhalira kuwuluka kapena namzeze wokhalira kuzungulirazungulira, ndi mmenenso limachitira temberero lopanda chifukwa, silichitika.

Onani mutuwo Koperani




Miyambo 26:2
10 Mawu Ofanana  

Kapena Yehova adzayang'anira chosayenerachi alikundichitira ine, ndipo Yehova adzandibwezera chabwino m'malo mwa kunditukwana kwa lero.


Yehova wabwezera pa iwe mwazi wonse wa nyumba ya Saulo, amene iwe wakhala mfumu m'malo mwake; ndipo Yehova wapereka ufumuwo m'dzanja la Abisalomu mwana wako; ndipo ona, wagwidwa m'kuipa kwako kwa iwe wekha, chifukwa uli munthu wa mwazi.


popeza sanawachingamire ana a Israele ndi chakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso.


Atemberere iwowa, koma mudalitse ndinu; pakuuka iwowa adzachita manyazi, koma mtumiki wanu adzakondwera.


Monga mbalame yosochera kuchisa chake, momwemo munthu wosochera kumalo ake.


Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.


Ndidzatemberera bwanji amene Mulungu sanamtemberere? Ndidzanyoza bwanji, amene Yehova sanamnyoze?


Ndipo Mfilisti anati kwa Davide, Ine ndine galu kodi, kuti iwe ukudza kwa ine ndi ndodo? Ndi Mfilistiyo anatukwana Davide natchula milungu yake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa