Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:33 - Buku Lopatulika

33 Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anachitenga, nachibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anachitenga, nachibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Yesu adaŵaphera fanizo linanso. Adati, “Ufumu wakumwamba ulinso ngati chofufumitsira buledi, chimene mai wina adachisanganiza ndi ufa wokwanira miyeso itatu, mpaka mtanda wonse udafufuma.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Iye anawawuzanso fanizo lina nati: “Ufumu wakumwamba ufanana ndi yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza mu ufa wambiri mpaka wonse unafufuma.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:33
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu analowa msanga m'hema wake kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate.


Chomwecho Aminoni anagona, nadzikokomeza alikudwala; ndipo pamene mfumu inadza kumuona, Aminoni anati kwa mfumuyo, Mulole Tamara mlongo wanga abwere ndi kundipangira timitanda tiwiri pamaso panga, kuti ndikadye cha m'manja mwake.


Koma wolungama asungitsa njira yake, ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.


Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.


Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matanda kucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.


Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake;


Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu mmodzi yense; koma chifukwa cha osankhidwa amene anawasankha, anafupikitsa masikuwo.


Ufanana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anatenga, nachibisa mu miyeso itatu ya ufa, kufikira unatupo wonsewo.


Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka.


Chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse.


pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;


Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chionjezere, m'chidziwitso, ndi kuzindikira konse;


Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.


Ndipo Gideoni analowa, nakonza kambuzi ndi mikate yopanda chotupitsa ya efa wa ufa; nyamayi anaiika m'lichero, ndi msuzi anauthira mumbale, natuluka nazo kwa Iye ali patsinde pa thundu, nazipereka.


Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng'ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye kunyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng'ono.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa