Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala mu Hazazoni-Tamara.
Numeri 13:29 - Buku Lopatulika Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aamaleke amakhala m'dziko lakumwera. Ahiti, Ayebusi ndi Aamori amakhala m'dziko lamapiri. Akanani amakhala m'mphepete mwa nyanja ndi m'mphepete mwa mtsinje wa Yordani.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aamaleki amakhala ku Negevi, Ahiti, Ayebusi ndi Aamori amakhala mʼdziko la mapiri ndipo Akanaani amakhala pafupi ndi nyanja, mʼmbali mwa Yorodani.” |
Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala mu Hazazoni-Tamara.
ndipo munampeza mtima wake wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zake; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama.
ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukutulutsani m'mazunzo a Aejipito, kukulowezani m'dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.
ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.
Potero Mose anawatuma azonde dziko la Kanani, nanena nao, Kwerani uko kumwera, nimukwere kumapiri;
Koma Kalebe anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene.
Koma Aamaleke ndi Akanani akhala m'chigwamo; tembenukani mawa, nimunke ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.
Pakuti Aamaleke ndi Akanani ali komweko patsogolo panu, ndipo mudzagwa ndi lupanga; popeza mwabwerera m'mbuyo osatsata Yehova, chifukwa chake Yehova sadzakhala nanu.
Pamenepo anatsika Aamaleke, ndi Akanani, akukhala m'phirimo nawakantha, nawapha kufikira ku Horoma.
Ndipo anayang'ana ku Amaleke, nanena fanizo lake, nati, Amaleke ndiye woyamba wa amitundu; koma chitsiriziro chake, adzaonongeka ku nthawi zonse.
koma muwaononge konse Ahiti, ndi Aamori, Akanani, ndi Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi; monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani;
Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu, ndipo atakataya amitundu ambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikulu ndi yamphamvu yoposa inu;
Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibiyoni, nauthira nkhondo.
Ndipo amuna a ku Gibiyoni anatumira Yoswa mau kuchigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.
Nati Yoswa, Ndi ichi mudzadziwa kuti Mulungu wamoyo ali pakati pa inu, ndi kuti adzapirikitsa ndithu pamaso panu Akanani, ndi Ahiti, ndi Ahivi, ndi Aperizi, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Ayebusi.
Ndipo kunali, pamene mafumu onse a Aamori okhala tsidya la kumadzulo la Yordani, ndi mafumu onse a Akanani okhala ku nyanja anamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a Yordani pamaso pa ana a Israele mpaka titaoloka, mtima wao unasungunuka, analibenso moyo chifukwa cha ana a Israele.
Ndipo kunali, pakumva ichi mafumu onse a tsidya ilo la Yordani, kumapiri ndi kuchidikha, ndi ku madooko onse a Nyanja Yaikulu, pandunji pa Lebanoni: Ahiti ndi Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;
Ndipo ana a Israele anakhala pakati pa Akanani, Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi;
Ndipo kunali, akabzala Israele, amakwera Amidiyani, ndi Amaleke, ndi ana a kum'mawa, inde amawakwerera;
Ndipo iye anakula mphamvu, nakantha Aamaleke, napulumutsa Aisraele m'manja a akuwawawanya.
Ndipo Davide ndi anthu ake anakwera, nathira nkhondo yovumbulukira pa Agesuri, ndi Agerizi, ndi Aamaleke; pakuti awa ndiwo anthu akale m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Ejipito.
Ndipo kunali, pakufika Davide ndi anthu ake ku Zikilagi tsiku lachitatu, Aamaleke adaponya nkhondo yovumbulukira kumwera, ndi ku Zikilagi, nathyola Zikilagi nautentha ndi moto;
Ndipo mizinda ya Israele imene Afilisti adailanda kale inabwezedwa kwa Aisraele, kuyambira ku Ekeroni kufikira ku Gati; ndi Aisraele analanditsa midzi yao m'manja a Afilisti. Ndipo pakati pa Aisraele ndi Aamori panali mtendere;