Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 13:28 - Buku Lopatulika

28 Komatu anthu okhala m'dzikomo ngamphamvu; ndi mizindayo nja malinga, yaikulu ndithu; ndipo tinaonakonso ana a Anaki.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Komatu anthu okhala m'dzikomo ngamphamvu; ndi midziyo nja malinga, yaikulu ndithu; ndipo tinaonakonso ana a Anaki.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Komatu anthu am'dzikomo ngamphamvu, mizinda yao ndi yozingidwa ndi malinga, ndiponso ndi yaikulu kwambiri. Kuwonjezera pamenepo, tidaonanso zidzukulu za Aanaki kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Koma anthu amene amakhala mʼdzikomo ndi amphamvu, mizinda yawo ndi ya malinga aakulu kwambiri. Tinaonanso Aanaki kumeneko.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 13:28
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide.


Tinaonakonso Anefili, ana a Anaki, obadwa ndi Anefili; ndipo tinaoneka m'maso mwathu ngati ziwala; momwemonso tinaoneka m'maso mwao.


Tikwere kuti? Abale athu atimyukitsa mitima yathu, ndi kuti, Anthuwo ndiwo aakulu ndi aatali akuposa ife; mizinda ndi yaikulu ndi ya malinga ofikira m'mwamba: tinaonakonso ana a Anaki.


ndiwo anthu aakulu, ndi ambiri, ndi ataliatali, monga Aanaki; koma Yehova anawaononga pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao;


Yonseyi ndiyo mizinda yozinga ndi malinga aatali, zitseko, ndi mipiringidzo; pamodzi ndi midzi yambirimbiri yopanda malinga.


Panalibe Aanaki otsala m'dziko la ana a Israele; koma mu Gaza ndi mu Gati ndi mu Asidodi anatsalamo ena.


Ndipo tsopano, ndipatseni phiri ili limene Yehova ananenera tsiku lija; pakuti udamva tsiku lijalo kuti Aanaki anali komweko, ndi mizinda yaikulu ndi yamalinga; kapena Yehova adzakhala ndi ine, kuti ndiwaingitse monga ananena Yehova.


Ndipo Kalebe anaingitsako ana aamuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.


Ndipo anapatsa Kalebe Hebroni monga Mose adanena; iye nawaingitsa komweko ana aamuna atatu a Anaki.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa