Eksodo 3:17 - Buku Lopatulika17 ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukutulutsani m'mazunzo a Aejipito, kukulowezani m'dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukutulutsani m'mazunzo a Aejipito, kukulowezani m'dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Mulungu watsimikiza kuti adzakutulutsani ku Ejipito kuno kumene mukuzunzika, ndipo adzakuloŵetsani m'dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Dzikolo ndi lamwanaalirenji.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Choncho wanenetsa kuti adzakutulutsani mʼdziko la Igupto, dziko la masautsoli kupita ku dziko la Akanaani, Ahiti, Aamori Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi, dziko loyenda mkaka ndi uchi.’ Onani mutuwo |
Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka mu Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi.