Eksodo 3:18 - Buku Lopatulika18 Ndipo adzamvera mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akulu a Israele, kwa mfumu ya Aejipito, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Ndipo adzamvera mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akulu a Israele, kwa mfumu ya Aejipito, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Mulungu adapitirira kunena kuti, “Zimene ukaŵauzezo, adzamva. Ndiye mukapite kwa mfumu ya ku Ejipito, iwe ndi atsogoleri a Aisraelewo, ndipo mfumuyo mukaiwuze kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Ahebri, adakumana nafe. Tsono tikukupemphani, mutilole kuti tipite ulendo wa masiku atatu ku chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wathu.’ Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 “Akuluakulu a Israeli akakumvera. Kenaka iwe ndi akuluakuluwo mukapite kwa mfumu ya Igupto ndipo mukanene kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri, wakumana nafe. Tsono tikukupemphani kuti mutilole tipite pa ulendo wa masiku atatu mʼchipululu kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.’ Onani mutuwo |