Eksodo 3:17 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Choncho wanenetsa kuti adzakutulutsani mʼdziko la Igupto, dziko la masautsoli kupita ku dziko la Akanaani, Ahiti, Aamori Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi, dziko loyenda mkaka ndi uchi.’ Onani mutuwoBuku Lopatulika17 ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukutulutsani m'mazunzo a Aejipito, kukulowezani m'dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukutulutsani m'mazunzo a Aejipito, kukulowezani m'dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Mulungu watsimikiza kuti adzakutulutsani ku Ejipito kuno kumene mukuzunzika, ndipo adzakuloŵetsani m'dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Dzikolo ndi lamwanaalirenji.” Onani mutuwo |
Aisraeli anakhala akuyenda mʼchipululu kwa zaka makumi anayi mpaka amuna onse amene potuluka mʼdziko la Igupto anali a msinkhu woyenera kupita ku nkhondo anamwalira. Iwo anafa chifukwa sanamvere mawu a Yehova. Yehova anawalumbirira kuti sadzalowa konse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi limene analonjeza kwa makolo awo kuti adzatipatsa.