Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 14:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala mu Hazazoni-Tamara.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala m'Hazazoni-Tamara.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ndipo adapotoloka, nakafika ku Enimisipati (ndiye kuti Kadesi), ndipo adagonjetsa dziko lonse la Aamaleke pamodzi ndi la Aamori amene ankakhala ku Hazazoni-Tamara.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Kenaka anabwerera napita ku Eni-Misipati (ku Kadesi), ndipo anagonjetsa dera lonse la Aamaleki, kuphatikizanso Aamori amene ankakhala ku Hazazoni Tamara.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 14:7
19 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake chitsimecho chinatchedwa Beere-Lahai-Roi; taonani chili pakati pa Kadesi ndi Beredi.


Abrahamu ndipo anachoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kadesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo mu Gerari.


Ndipo Timna anali mkazi wake wamng'ono wa Elifazi mwana wamwamuna wa Esau; ndipo anambalira Elifazi Amaleke: amenewa ndi ana aamuna a Ada mkazi wake wa Esau.


mfumu Kora, mfumu Gatamu, mfumu Amaleke: amenewa ndi mafumu a kwa Elifazi m'dziko la Edomu: amenewa ndi ana aamuna a Ada.


Pamenepo anadza anthu akuuza Yehosafati, kuti, Ukudzerani unyinji waukulu wa anthu ochokera tsidya la nyanja ku Aramu; ndipo taonani, ali ku Hazazoni-Tamara, ndiwo Engedi.


Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za mu Nyanja Yaikulu, zambirimbiri.


Ndi ku malire a Gadi, mbali ya kumwera, kuloza kumwera, malire akhale kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, kufikira ku Nyanja Yaikulu.


Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israele, ku chipululu cha Parani ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.


Pakuti Aamaleke ndi Akanani ali komweko patsogolo panu, ndipo mudzagwa ndi lupanga; popeza mwabwerera m'mbuyo osatsata Yehova, chifukwa chake Yehova sadzakhala nanu.


Pamenepo anatsika Aamaleke, ndi Akanani, akukhala m'phirimo nawakantha, nawapha kufikira ku Horoma.


Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m'chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala mu Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko.


Ndipo anayang'ana ku Amaleke, nanena fanizo lake, nati, Amaleke ndiye woyamba wa amitundu; koma chitsiriziro chake, adzaonongeka ku nthawi zonse.


Pamenepo tinayenda ulendo kuchokera ku Horebu, ndi kubzola m'chipululu chachikulu ndi choopsa chija chonse munachionachi, panjira ya ku mapiri a Aamori, monga Yehova Mulungu wathu anatiuza; ndipo tinadza ku Kadesi-Baranea.


Potero munakhala mu Kadesi masiku ambiri, monga mwa masiku munakhalako.


ndi Nibisani, ndi Mzinda wa Mchere, ndi Engedi; mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa