Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 10:5 - Buku Lopatulika

5 Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibiyoni, nauthira nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibiyoni, nauthira nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mafumu asanu a Aamoriwo, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi ndiponso ya ku Egiloni, adagwirizana. Adasonkhanitsa ankhondo ao nazinga mzinda wa Gibiyoni, ndi kuuthira nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mafumu asanu a Aamori aja, mfumu ya Yerusalemu, mfumu ya Hebroni, mfumu ya Yarimuti, mfumu ya Lakisi ndi mfumu ya Egiloni, anagwirizana. Iwo anasonkhanitsa ankhondo awo nazungulira mzinda wa Gibiyoni ndi kuwuthira nkhondo.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 10:5
8 Mawu Ofanana  

Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wachinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe.


pamene nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni inamenyana ndi Yerusalemu, ndi mizinda yonse ya Yuda imene inatsala, ndi Lakisi ndi Azeka; pakuti mizinda ya Yuda yamalinga yotsala ndi imeneyi.


Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordani.


Ndipo mafumu awa asanu anathawa, nabisala m'phanga la ku Makeda.


Ndipo amuna a ku Gibiyoni anatumira Yoswa mau kuchigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.


Ndipo mizinda ya Israele imene Afilisti adailanda kale inabwezedwa kwa Aisraele, kuyambira ku Ekeroni kufikira ku Gati; ndi Aisraele analanditsa midzi yao m'manja a Afilisti. Ndipo pakati pa Aisraele ndi Aamori panali mtendere;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa